M’modzi mwa anthu otsatira chipani cha United Democratic Front ( UDF) , bambo John Black Dzuwa athokoza Pulezidenti wachipani cha Malawi Congress Party ( MCP) His Excellency Dr Lazarus McCarthy Chakwera yemwenso ndi Pulezidenti wadziko lino kaamba kolola kuti milandu ya Pulezidenti wakale wadziko lino Dr Bakili Muluzi ithe. Makhothi adziko lino athetsa milando yonse ya Dr Bakili Bakili Muluzi. Bambo John Black Dzuwa ati , Dr Bakili Muluzi adamangidwa kaamba kandale. A John Black Dzuwa atinso akuthokoza kuti dziko lapansi kuli anthu omwe amamva zinthu ndikupanga kuti Zikhale bwino. A John Black Dzuwa ati sadakhulupilire komanso kuyembekezera kuti chipani chomwe chingadzamasule Dr Bakili Muluzi mkukhala MCP. A John Black Dzuwa akuthokoza Pulezidenti wa MCP ( Dr Lazarus McCarthy Chakwera) komanso akuthokoza akuluakulu akumakhothi kaamba kothetsa milandu ya Atcheya His Excellency Dr Bakili Muluzi. Adzuwa akuti Zikomo !
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!