Kwimbi la Asilamu lasonkhana kuchita mapemphero pa bwalo la sukulu ya Mufti Abbassi ku Mangochi pambuyo pakutsiliza kusala kudya kwa masiku asanu ndi anayi.
Munyengoyi, asilamu amapha nyama ndikugawila anthu ena osowa, ngati njira imodzi yochita zachifundo.
Eid Mubarak iyi ndiyosiyanilapo ndi ija magulu ena a Chisilamu amasemphana pa tsiku lomwe mwezi waonekela.