Woyimbira Sadali Bwino

Mphunzitsi wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets wadandaula ndi kaimbilidwa komwe kadalipo masewero awo ndi timu ya Red Arrows loweruka lapitali.

Callisto Pasuwa wati ziganizo zina zomwe adachita oyimbira masewerowa ndi zomwe zidachititsa kuti timuyi igonje.

Pasuwa wapempha kuti chilungamo chidzikhalapo pa masewero ndi cholinga chakuti mpikisano udzikhala okomera matimu onse.

Elmabrouk Muhamad wa ku Libya ndi yemwe adaimbira masewero achibwereza omwe Bullets idagonja 2-0 pa bwalo la Heroes m’dziko la Zambia.

Kutsatira kugonjaku, Bullets idatuluka mpikisanowu 3-2 pa masewero awiri.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Please disable your adblocker or whitelist this site!