Mphunzitsi wamkulu watimu ya Flames Patrick Mabedi wapempha nzika zadziko lino kuti ziwayikize mu mapemphero ati pofuna kupeza chipambano mumasewero awo mawa ndi Burkina Faso mumasewero ofuna kudzigulira malo ku ndime yotsiliza ya Africa Cup of Nations ( AFCON) omwe achitikire ku Mali.
Mabedi wati timu yake ikamapita mumasewerowa ifunitsitsa kupeza chipambano ati pofuna kuziziritsa mitima ya a Malawi kutsatira chigonjetso cha 3-2 chomwe anapeza ndi Burundi sabata yatha mumasewero enaso amu gulu L a mpikisanowu.
Iye wati mawa pofuna kulanga timu ya Burkina Faso awonetsetsa kuti osewera ake akupita pafupi pafupi kugolo la adani awo.
Padakali pano timu ya Malawi mu gulu L ilibe point iliyonse pomwe Burkina Faso ili ndi point imodzi kuchoka mumasewero amodzi omwe matimu onse asewera.
Kuchokera mu mchaka cha 2000 timu ya Malawi ndi Burkina Faso akumana kokwana kasanu ndi kamodzi ndipo timu yadziko lino sinayambe yapambanapo koma yagonja ka nayi kufananitsa mphamvu kawiri.
Za uzimu tsopano