Dedza ikuyenera kupisa m’thumba kuti ipereke K10 million, pamene Wanderers ilipira K4 million pa nkhani ya Kamwendo
Football Association of Malawi (FAM) kudzera ku komiti yomwe imaunika nkhani yokhudza osewera kutsogola, Promise Kamwendo, yagamula timu ya Premier Bet Dedza Dynamos kuti ibweze ndalama zokwana K3 million komanso K4 million zomwe inalandira kuchokera ku matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Mighty Mukuru Wanderers.
Izi zikudza kutsatira kuunika kwakuya kwa nkhani ya osewerayu yemwe anasainira mgwirizano wa zaka zitatu ndi Manoma ngakhale amayenera ku lowera ku Mapale potengera kuti anali atalipira kale ndalama za osewerayu.
Komitiyi yalamulanso kuti Kamwendo abweze ndalama zokwana K6 million zomwe analandira ku Lali Luban paza m’gwirizano wawo kamba ka kontirakiti yomwe anasainira.
Mighty Mukuru Wanderers ayipeza yolakwa ndipo yauzidwa kuti ilipire ndalama zokwana K4 million kamba ka madulira pa nkhani yokhudza kusaina osewera.
Malingana ndi chigamulochi, Dedza ailipiritsa ndalama zokwana K3 million kamba kofuna kudya mbali zonse ziwiri zomwe ndi zolakwika pa ndondomeko yofuna kugulitsa osewera.
FAM yalamulanso kuti osewerayu abwelere ndikukayambiranso kutumikira timu ya Dedza potengera kuti yathetsa mgwirizano omwe anasainira ndi Manoma.
Komitiyi yapereka masiku atatu kumbali zokhudzidwa pa chigamulochi.