Mphunzitsi wamkulu wa timu ya Flames Patrick Mabedi wati timuyi ili ndi mwayi ochepa tsopano oti ikhoza kudzipezera malo ku ndime yotsiliza yampikisanowa Africa Cup of Nations (AFCON) omwe ukachitikire mdziko la Morocco chaka cha mawa.
Mabedi wayankhula mawuwa kutsatira timuyi itagonja ndi zigoli zitatu kwa chimodzi ndi timu ya Burkina Faso mdziko la Mali mumasewero awo achiwiri ofuna kudzipezera malo ku ndime yotsilizayi.
Mabedi wati kunena mwachilungamo kutaya kwa ma points 6 mumasewero awiri omwe asewera ndi zokayikitsa kuti ndikukhala ndi umwayi ochita bwino mumasewero omwe atsala pomwe matimu azawo mugululi atola kale ma points.
Mphunzitsiyu wati timuyi lachiwiri sinachite bwino ati kaamba kosowa mwambo kwa osewera ake omwe sanavere uphungu omwe anawapatsa momwe angayigonjetsere Burkina Faso.
Timu ya Burkina Faso ndi yomwe ikutsogola mugulu L ndi ma points 4 pomwe Senegal ikubwera panambala ya chiwiri ndi ma points anayi koma zigoli zomwe zikuwasiyanitsa pomwe Burundi ili panambala 3 ndi ma points atatu kuchoka mumasewero awiri omwe matimu onse asewera.
Wolemba : Eliot Tandani