Katswiri pa nkhani za masewero a Humphreys Mvula wati sakugwirizanabe ndi mphunzitsi wamkulu watimu ya Flames Patrick Mabedi pomamusiya Gabadinho Mhango mumasewero ake osiyanasiyana pomati wakula.
A Mvula ati Mabedi akuyenera kuganizira bwino pa za osewera wa Marumo Gallants-yu pomwe iwo akuti sakukhulupilira zoti Mhango anatha kuti sangatumikire timu yadziko lino.
A Mvula ati timu yadziko lino ikufunika kuyimanga ndi osewera omwe ndi akuluakulu komanso ena achisodzera pofuna kuti awa obwera kumene adziphunzira kwa akalewa.
Mphunzitsi Mabedi sabata yatha anawuza olemba nkhani kuti iye alibe zotsamwitsa zili zonse ndi Mhango posamutenga mumasewero atimuyi ndi Burundi komanso Burkina Faso mumpikisano ofuna kudzipezera malo kundime yotsiliza ya Africa Cup of Nations.