Tisiye kuloza chala a Mabedi-Mpima

Bungwe la aphunzitsi a mpira wamiyendo m’dziko muno lati silikugwilizana ndi anthu omwe akuloza chala mphunzitsi wa timuyi, Patrick Mabedi, kuti walephera ntchito yake.Tinene chalungamo mwayi wathu ndiwochepa tsopano opita ku AFCON – watero Mabedi

Izi zikutsatira kulephera kuchita bwino kwa Flames pomwe inagonja pa khomo ndi timu ya Burundi 1-0 pa bwalo la Bingu mu nzinda wa Lilongwe, komanso 3-2 ndi timu ya Burkina Faso ku Bamako m’dziko la Mali mumpikisano wa Africa Cup of Nations (AFCON).Mend Fences With Gaba -Kinnah Phiri advise Mabedi

Mlembi wa bungweli, Dave Mpima, wati kulankhula zonyoza Mabedi sizithandiza kanthu koma kuti mbali zokhudzidwa zikhale pansi ndikupeza njira yoti timuyi iyambirenso kuchita bwino ngati momwe zinaliri m’zaka za 1987 komanso 1988.

Malawi ili pansi mu gulu potengera kuti ilibe chipambano china chilichonse.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *