Silver Strikers Yagonjesa Premier Bet Dedza Dynamos

FB IMG 1726732233235

Timu ya Silver Strikers yapereka ubatizo wa zigoli ku timu ya Premier Bet Dedza Dynamos mu mpikisano wa Airtel Top 8 pa bwalo la Silver mu nzinda wa Lilongwe.

Anayambitsa zonse anali Chimwemwe Idana ndipo Zebron Kalima anamwetsanso chimodzi asanabwere Chinsinsi Maonga kudzayedzeka zake ziwiri.

Ndipo Chifuniro Mpinganjira anamwetsa Chigoli chokhacho cha timu ya Dedza Dynamos.

Atatha masewerowa Mphunzitsi wamkulu Wa Silver Strikers, Peter Mponda, wati ndiokhutira ndi kupambanaku komanso momwe osewera ake anachitira.

”Anyamata anamva zomwe tinakambirana tisanabwere mu masewerowa ndipo ndiyamikire kuti achita bwino pochinya zigoli zambiri komanso kusewera bwino,” watero Mponda.

M’mau ake Mphunzitsi wamkulu wa Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati sizinayende momwe anakonzekera chifukwa anachinyitsa m’sanga komanso chigoli chachiwiri chomwe ndichokaikitsa chinasokoneza osewera ake.

‘Tagonja koma sikuti tathera pamenepa tikayesesa masewero a chibwereza kukachinya komanso kuteteza bwino kuti tikathe kufika ndime ina,” watero Bunya.

Kalima ndiye anasankhidwa kukhala dolo mbambande kuposa onse mumasewerowa.

Masewero a chibwereza alipo pa 20 October pa bwalo la Dedza.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *