Sindingapepese chifukwa Dambwe ndi malo Amizimu Yakufa, Nanga Ndikapepese ziwanda? – Enock Kanzingeni Chihana

“Sindingawope chifukwa ndimayankhulira aMalawi osauka komanso chipani!

Ulamuliro opanda masomphenya omwe ukutsogozedwa ndi mizimu yoyipa ukuyesera kuzunza anthu osalakwa kuti ukachite ufumu pamaso pa amphawi mu dziko la democracy!

Dambwe ndi malo a mizimu yakufa osati anthu amoyo!

Aliyense oyankhula m’malo mwa ziwanda sachita cholungama konse.

Ngati ndalakwira mizimu ndipo iyo imamva nayiyankhula iloreni tiyankhulane koma sindingapepetse munthu otumikira chinthu chopanda moyo!

Nanenso ndine mchewa ndipo tanthawuzo loti ndabwe ndimaliziwa kuti ndi dziko la mizimu yopanda moyo.

Ndikunenetsa molimba mtima mu dzina la YESU MKHRISTU mwana wa MULUNGU WAMOYO kuti sindingapepetse mizimu yopanda moyo chifukwa iyo ikuyenera kupita ku chiwonongeko pamodzi ndi ntchito zake zoyipa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *