‘A Kabambe sakudziwa chomwe akunena’ _ Kumkuyu

Nduna yofalitsa nkhani yemwenso ndi mneneri waboma Moses Kumkuyu wati zomwe wayankhula mtsogoleri wachipani cha UTM dzulo pamsonkhano wa atolankhani zikuonetselatu kuti sadziwa momwe boma limayendera.

Dzulo a Kabambe anadzudzula mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera ponena kuti akungokhalira kupempha thandizo mmaiko akunja zomwe akuti wasandutsa a Malawi ambiri kukhala ‘a Lazalo opemphapempha’.

Komatu mneneri wabomayu wati a Kabambe angowonetselatu kuti ndi munthu yemwe sakudziwa momwe kayendetsedwe kaboma kamakhalira.

“Zomwe ayankhula abambo amene aja sizoona. Dziko lino lili mugulu la maiko osaukitsitsa ndipo kuti titulukemo tikuyenera ndithu kuti anzathu atigwire dzanja.

“Komansotu sichanzeru kuti mtsogoleri azilephera kupempha thandizo pomwe anthu mdziko lake akufa ndi njala ati poopa kuti anthu amuseka kuti akupempha kwambiri. Limenelo ndi thamo. Tsono mtsogoleri asamakhale wathamo.” Watelo Kumkuyu.

Mwazina a Kabambe anati iwo akadzalowa m’boma chaka chamawa adzaonetsetsa kuti akuika ndalama kuntchito yotukula dziko lino ndipo azidzalolera kuyenda wapansi bola ntchito zachitukuko zikupita patsogolo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *