BWATO SATSITSILANA PAKATI PA NYANJA”-Micheal Usi

Nduna yowona zokopa alendo yomwenso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha UTM, Michael Usi awuza President Lazarus chakwera kuti chipani cha UTM chilibe lingaliro lotuluka mu mgwilizano wa Tonse alliance ngakhale pali kagulu kena komwe kakufuna zinthu zitero.

A Usi ati kukakamiza chipani cha UTM kutuluka mu mgwilizano wa Tonse mchimodzimodzi kukakamiza munthu kuti atsike mu bwato lili pakati pa nyanja.

A Usi alumbila ponena kuti UTM ipitiliza kulemekeza mgwilizano wa Tonse.

Iwo ayankhula izi pa mwambo okumbukira mtsogoleri oyamba wa dziko lino Dr Hastings Kamuzu Banda Ku Lilongwe.

Poyankhulapo, ndunayi inauzanso Dr chakwera kuti achotse ntchito kagulu kena ka anthu komwe kakufuna kusokoneza boma lake.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *