Olemba, Yusuf Daisa
Anthu a mdera la Mangochi Masongola kwa Senior Chief Jalasi, ayamikira Ali Blessings Idi yemwe akupikisana paudindo wa phungu wakunyumba yamalamulo, chifukwa chogawa ufa ku mabanja 500 omwe akuvutika ndinjala yomwe yavuta mdziko muno.
Polakhula ndi anthu omwe anasonkhana pa bwalo la m’mudzi wa amfumu Namamba, nyakwawa yayikulu Namamba yayamikira khalidwe la Idi lothandiza anthu ovutika pomwe ali pamavuto.
Mfumuyi yati khalidwe ili ndi lomwe akulifuna kwa phungu wa derali, oti amasamala komanso kukumbukira anthu akumudzi pamavuto komanso pomwe pano chakudya chakwera mtengo pa msika.
Iyo yati, kukwera kwa zinthu pansika kwapangitsa kuti anthu a kumudzi azigona ndi njala chifukwa sakufikira mitengo yokwerayi.
Poonjezera, Saujati Mussah ochokera dera la Kwiputi, wati anthu ambiri akugona ndi njala kamba koti akusowa ndalama yogulira chakudya chomwe chikudula pakadali pano.
“Mvula chaka chino yachita njomba, ndipo chimanga m’minda yambiri sichinachite bwino, koma ndinjalayi takakamizika kudya chachiwisi komanso maungu osakhwima. Izizi ndikuona kuti chaka chinonso njala ipitilira chifukwa tizakolora chimanga chochepa,” watero Mussah.
Iye kotero wati pomwe walandira ufawu, akaphikira ana nsima yomwe anaisowa kwanthawi yaitali.
Naye Lucy Saidi ochokera m’mudzi wa Nkweya, anali osangalala polandira ufawu, ndipo anatsindika zokhala ndi Atsongoleri ngati Idi omwe amasamala mavuto a wanthu akumudzi.
” Ineyo nkoyamba kulandira ufa, ndipo izi sindinazionepo. Dela lino limasowekwera atsogoleri omwe amathandiza anthu akumudzi pomwe ali pamavuto, ngati m’mene akuchitira Idi,” watero Saidi.
Iye kotero wapempha Idi kuti apitirize mtima othandiza anthu akuders la Mangochi Masongola.
M’mau ake Idi wasindika zakhumbo lake lofuna kuthandiza komanso kutukula dera la Mangochi Masongola.
Iye wati apitiriza kuthandiza anthuwa powapatsa zosowa zawo monga chakudya, madzi abwino, chithandizo cha zaumoyo, komanso maphunziro kuti umoyo wawo utukuke.
Aka sikoyamba Idi kufikira anthu ovutika kuderali , pomwe m’mbuyomu wafikiranso mabanja okwana 400 ndichakudya.
.