Mon. Apr 29th, 2024

A Malawi ambiri asauka kwambiri chaka chino mdziko muno kusiyana ndi chaka chatha, yatero World Bank

Banki yaikulu pa dziko lonse ya World Bank yati chiwelengelo cha anthu osaukitsitsa chipitilila kuchuluka m’dziko muno ndi ma pelecenti 71.7 m’chaka cha 2023 kufika pa 72 pelecenti m’chaka cha 2024.

Umphawi ndi usiwa
Izi ndi malingana ndi kafukufuku yemwe banki-yi yachita ontchedwa Macro Poverty Outlook yemwe watuluka sabata yatha.

Kafukufuku-yu akupeleka chithunzithunzi cha momwe mavuto alili komanso chitukuko pa khani ya zachuma ku maiko 48 omwe akungotuka kumene kuno ku Africa.

Kafukufuku-yu amatulutsidwa kawili pa chaka ku mikumano ya banki yaikulu pa dziko lonse.

Kafukufuku-yu wafotokozela kuti kuchuluka kwa kusowa kwa chakudya, komwe kukudza chifukwa cha kukwela mitengo kwa chakudya-chi zomwe zipangitsanso kuti kukhale zokolola zikhale zochepa ndipo izi ndi zomwe zitachititse kuti uphawi uchulukile dziko muno.

Malingana ndi kafukufuku chuma cha Malawi chikuyembekezeka kukwela ndi ma pelecenti awili mu chaka cha 2024.

“Kuchepekedwa kwa zipangizo za ulimi ndi kusitha kwa nyengo komwe kwadza mu nyengo yolima kuchepetsa zokolola. Kusithasitha kwa mitengo yogulila zithu ku misika ya maiko a kunja, zikuyembekeza kukhudzanso kagulidwe ka katundu kuchokela m’maiko a kunja ndi kayendetsedwe ka ntchito za chuma mu makampani, ” kafukufuku-yu akufotokoza.

Bungwe lotchedwa Bretton Woods laonjezela kunena kuti kagulidwe ka katundu kakuyembekezeka kukhalabe kokwela ndi ma pelecenti opitilila 27 m’chaka cha 2024, potengela kuti njila zochepetsela mitengo ya katundu zikhudzidwa ndi momwe chuma chikuyendetsedwela kaamba ka kuchepa kwa zokolola ndi kukwela cha chakudya.

“Kukwela kwa zithu zongwilitsa ntchito mphamvu za magetsi Kafukufuku kwadza kaamba ka kukwela kwa ndalama ya kwacha kupitiliza kukolezela kwa kukwela kwa katundu.

Chuma chikuyembekezeka kufika pa 21.5 pelecenti mu 2024-2025. Izi zikhala chonchi kaamba ka kukwela kwa misokho yomwe dziko lino likuyembekezeka kutolela komanso kukwela kwa thandizo lomwe dziko lino likuyenela kukhala nako, lomwe likuyembekezeka kufika pa 5.4 pelecenti pa chaka, zomwe ndizokwela mu dzaka khumi zapitazo,” banki yaikulu pa dziko lonse yafotokoza motelo.

Malingana ndi kafukufuku kagwilitsidwe ntchito ka ndalama kakuyembekezeka kufika pa 28.4 pelecenti pa chaka zomwe zikutathauzila kuti pakhala kuchepa kwa 6.6 pelecenti pa ndalama zomwe zikuyembezedwa kugwilitsidwa ntchito mu chaka cha 2024-2025 cha boma.

Banki-yi yafotokoza kuti kulephela kutolela misokho yokwanila komanso kuchulutsa kagwilitsidwe ntchito ka ndalama zipitiliza kuchulukitsa kwa ngongole zomwe dziko lino lilinazo.

“Kugula kwa katundu kunja kukuyembekezeka kukwela kaamba ka kuchuluka kwa zochudya zomwe zikufunika kuti zigulidwe maiko a kunja kuti dziko lino lithane ndi mavuto a chakudya.

“Pamene kutumiza kwa katundu kuja kukuyembekezeka kubwelela m’chimake, mavuto omwe adza pa khani ya zaulimi chifukwa cha kusitha wa nyengo atha kudzetsa mavuto pa khani yotumiza katundu kuja. Kuchepekedwa pa khani ya za chuma kukuyembekezeka kukhalabe kokwela kufikila pa 20 pelecenti pa chaka,” Kafukufuku-yu wafotokozela.

Pothililapo ndimanga pa kukwela kwa mavuto a zachuma, katswili wa zachuma yemwe akukhala dziko la Scotland Velli Nyirongo mavuto omwe dziko la Malawi likukumana nawo pa khani ya za chuma akupangitsa kuti dziko la Malawi lisapite patsogolo.

“Zikungotathauza kuti dziko likukanika kuchotsa anthu ake mu umphawi. Kuti tione kusitha kwekweni zikufunika kuti pakhale kukwela kwa chuma kolongosoka kufikila pa 6 pelecenti pa chaka, pali zithu zochepa zomwe tikuyenela kuziyang’anitsitsa kuti tithane ndi mavuto amenewa.

Kuthana ndi khani ya kugula komanso kugulitsa katundu ndi kovuta. Dziko la Malawi likuyenela kumatumiza katundu wambili osati kugula katundu wambili ndipo izi zibweletsa ndalama za maiko ena zochuluka zomwe zikuchulukitse chuma cha dziko lino. Dziko la Malawi limadalila kwambili pa ulimi zomwe anthu ochuluka dziko lino zikuwapindulila koma izi zakhala zili zovuta kaamba ka kusitha kwa nyengo. Kusitha pa njila zopezela chuma komanso kuchulukitsa kwa ntchito mu madela ena ndi zofunika,” Nyirongo anafotokoza.

Iye anatinso kuchuluka kwa anthu ndi khani inanso yomwe ikuyenela kuiyang’ana.

“Kuchuluka kwa anthu m’dziko muno kukuposa kuthekela komwe dziko lino lilinako kuti lithe kuthandiza aliyense. Izi zikuyenela kuyang’anidwa. Kuika chuma chochuluka kumaphunzilo ndizofunikila kuti dziko lidzakhala lotukuka m’tsogolomu, komanso kuonetsetsa kuti chakudya ndichokwanila ndi chithunso chofunikila, dziko ngati Malawi silikufunika kumadalila chakudya chochita kugula maiko ena pomwe lili ndi kuthekela kokhala lodzidalila pa khani ya chakudya,” Nyirongo anaonjezela.

Nduna ya za chuma Simplex Chithyola Banda sanapezeke kuti ayikilepo ndemanga pa khani-yi.
“`

Related Posts

The British NCA Operations In Malawi Remain Questionable, Britons Aim To Topple Tonse Government

Exposed! British NCA bankrolls PIJ to victimize successful business persons, politicians, judges in Malawi The truth be told! The establishment Read more

Mirece supports land reclamation bought by foreigners

Reverend Flywell Somanje…. this is the way to go A governance and human rights organization, the Millennium Information and Resource Read more

Paramount Holdings Donates Medical Equipments To Area 25 Health Centre

Paramount Holdings Limited has handed over medical equipment worth 3 million Kwacha to Area 25 health centre. The organisation's Operations Read more

I am not a crook— Mulli

MAINTAINED THAT PROCEDURES WERE FOLLOWED—Mulli— Picture by Catherine Maulidi Businessperson and National Bus Services Chairperson Leston Mulli on Tuesday told Read more

Other stories

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Ekhaya luxury Resort fully open