Boma Likufuna Kuthetsa Nkhanza Zomwe A Traffic Akumachita Mudziko Lino

Boma sopano lazindikila zoti a traffic ambili akugwila ntchito ndi akuluakulu achipani cha DPP kuti awononge mbiri ndikuligwesa.

Pofuna kuwonesa kuti eni magalimoto maka eni ma minibus sakuchitidwa nkhaza boma sopano layamba kufufuza apolice a traffic omwe akumagwila magalimoto mwachisawawa maka omwe akumakhala nditimilandu tating’ono kwambili monga kuyiwala ma triangle plates.

Kafukufukuyi akuza antolankhani a Malawians News Online atabwelesa poyela malipoti onena kuti a traffic ambili maka omwe akumayima mumadela ozungulira mzinda wa Blantyre, Lilongwe ndi Chiradzulu akumachitila nkhanza oyendesa ma minbus komanso magalimoto ang’onoang’ono pomawalipilitsa ndalama zambili zedi pamilandu yaying’ono kwambili yomwe akanangotha kuwapasa chenjezo.

Milandu Yoyenera kulipira pa Nsewu ndi Iyi

Milandu yoyenela kugwidwa pansewu imayenela kukhala ikuluikulu monga kuyendesa galimoto opanda Insurance, Licence, COF, Overload ndikuyendesa galimoto utalezela kapena galimoto yamatayala.

Milandu ing’onoing’ono a traffic amangoyelenela kupeleka chenjezo basi osati mpaka kugwila ndikudulira ma driver lisiti ya K10 000 kuti akalipile.

Nkhanza zomwe a traffic amenewa akuchita ndizosayenela mudziko lino kamba koti zikusoneza kwambili ubale wa anthu, eni magalimoto ndi boma.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *