Buluma Wasiya Ntchito Ndipo Wayamba Kuulula Zobisika

Yemwe amagwirizira ngati mkulu wa bungwe la NOCMA, Hellen Buluma watula pansi udindo-wu koma waulula zina zobisika zomwe akuti akuluakulu ena m’boma komanso andale akhala akumukakamiza kuchita ngakhale nzosemphana ndi malamulo.

Izi zili mukalata yopuma pa ntchito yomwe a Buluma alembera wapampando wa board ya bungweli, Colleen Zamba, yemwenso ndi mlembi mu ofesi ya mtsogoleri wa dziko ndi nduna zake.

ABuluma ati a Zamba komanso mlembi ku unduna waza mphamvu, Alfonso Chikuni komanso andale ena akhala akuwapanikiza komanso kuwaopseza kuti apereke ma contract mwa chinyengo ku kampani za ku mtima kwa adindowa.

Mu kalata yomwe taona, a Buluma atinso akhala akuwakakamiza kuti apereke malo a Chipoka ku Salima kwa mkulu wina wa ndale m’chipani cha MCP kuti adzichita malonda koma mwautambwali ndi ochita malonda ena akunja.

“Mtsogoleri wadziko lino wakhala akulankhula motsutsana ndi m’chitidwe-wu ndipo adandilangiza kuti ndidzichita zinthu nthawi zonse molingana ndi malamulo pogwira ntchito. Koma inu madam mwakhala mukundipanikiza ndi zosiyana ndi zomwe a pulezidenti amanena maka pa nkhani yolowelera pa ntchito,” yatero kalatayi.

Mai Zamba atsimikiza za kusiya ntchito kwa a Buluma koma sadafotokoze zambiri pomwe a Buluma sayankhe pomwe timafuna kumva zambiri kuchokera kea iwo pa nkhani-yi.

Izi zadza pomwe board ya NOCMA yakhala ikunyozera kumvera zomwe ofesi ya Ombudsman idanena kuti ichotse ntchito mai Buluma ati kamba koti panalibe kutsatira ndondomeko komanso malamulo pa nthawi yomwe ankawalemba ntchito.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *