Chakwera Aonetse Kuti Siwolephera Kutumikira A Malawi

Mabungwe omwe si aboma ku Kasungu ati nthawi yakwana tsopano kuti mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera aonetse kuti siwolephera kutumikira a Malawi.

Wapampando wa mabungwewa a Braxton Banda wati a Chakwera akuyenera kuchotsa ntchito mkulu wa nthambi ya immigration a Charles Kalumbo pa chimpwirikiti chokhudza ma passport.

A Banda akukhulupilira kuti izi zithandizira kuti anthu asataye chikhulupiliro mwa utsogoleri wa a Chakwera maka pomwe chisankho cha chaka cha mawa chayamba kale kununkhira.

“Kulephera kulondoloza ndikupezanso mayankho a vuto lomwe lili ku nthambi ya immigration, anthu ena akuloza chala mtsogoleri wa dziko linoyu.

“Ichi ndi chifukwa chake ife a mabungwe tikuwapempha komanso kuwatsina khutu a pulezidenti kuti achotse ntchito mkuluyu, pofuna kuteteza mbiri yawo komanso kukonza zinthu,” atero a Banda.

Pempholi ladza pomwe gulu lina la mzika zokhudziwa zakonza m’bindikiro ku ofesi za immigration pa 12 March pofuna kukamiza a Chakwera kuti achotse ntchito a Kalumo komanso nduna ya chitetezo a Ken Zikhale Ng’oma pa nkhani yomweyi.

Koma akuluakulu ku nthambi ya immigration ati akuyesetsa kuti athane ndi vutoli asanathe masiku 21 omwe a Chakwera adawapatsa kuti akonze zinthu..

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *