Chakwera Atsitse Mtengo Wa Fertiliser Kuchoka Pa k15,000 Kufika Pa k7500

1 min read

Bungwe la CDEDI Malawi lalamula kuti mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera atsitse mtengo wafeteleza yemwe ali pansi pa zipangizo za ulimi zotsika mtengo.

Mkulu wa bungwe la CDEDI Sylvester Namiwa amalankhula ndi atolankhani lachinayi mumzinda wa Lilongwe.

Malingana ndi Namiwa, a Chakwera akuyenera kutsitsa mtengo wafetelezayu kuchoka pa MK15 000 kufika pa MK7500 pathumba asanakhazikitse ndondomeko yogulira zipangizo za ulimi zotsika mtengo pa 21 November.

Mtsogoleri wabungwe la CDEDI-yu wachenjezanso boma kuti lisagulitse feteleza amene dziko la Malawi lalandira ngati thandizo kuchokera ku maiko ena, ndipo mmalo mwake agawe wa ulele kwa a Malawi.

A Namiwa alamulanso boma kuti litsekule misika yonse ya Admarc ndicholinga chakuti a Malawi asavutike kugula zipangizo za ulimi zotsika mtengo chaka chino.

You May Also Like

More From Author

+ There are no comments

Add yours