Saturday, April 13
Shadow

Chakwera Muzimuunikira Chilungamo Asanayankhule Kwa A Malawi

CHAKWERA MUDZIMUUNIKIRA MWACHILUNGAMO ASANALANKHULE KU MTUNDU WA A MALAWI ATERO AKATSWIRI KUUZA ALANGIZI A PUREZIDENTI

M’modzi mwa anthu omwe amayankhulapo pa zochitika m’dziko wapempha alangizi a mtsogoleri wa dziko lino kuti adzimuunikira mtsogoleriyu mwachilungamo.

A Lyford Chadza anena izi kutsatira zomwe wachita mtsogoleri wa dziko linoyu polengeza kuti dziko lino lili pa ngozi ya njala.

Iwo ati izi zimayenera kuchitika kale kale koma pomwe mitengo ya chimanga inakwera kwambiri kufikira thumba la chimanga kufika pa 55 sauzande kwacha.

A Chadza ati pa nthawi iyi anthu ena amakakamira kumafotokoza kuti m’dziko muno chimanga chilipo chokwanira.

Iwo ati zomwe adachita wa pa mpando wa komiti ya za ulimi ku nyumba ya malamulo a Sameer Suleiman masiku apitawa pofotokoza kuti m’dziko muno mulibe chimanga zitha kukhala kuti zidapereka chithunzithunzi chenicheni kwa Dr Chakwera ngakhale kuti iwo adakakamizidwa kuti abwenze mawuwa.

M’mawu ake ku uthenga opita ku mtundu wa amalawi, Dr Chakwera anati anayenda ndi kudzionera okha momwe anthu akuvutikira m’dziko muno.

See also  Tidkira Tsiku Lomwe Ayambe Kupanga Zipatso Zoyendera-CDEDI

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

President Lazarus Chakwera has officially opened the Blantyre International Cancer Centre, The private health facility, has been constructed by the Thomson and Barbara Mpinganjira Foundation