Nyumba Ya Malamulo Yakambirana Za Chamba

Aphungu akambirana ndi kuvomereza kuti pakhale lamulo loloreza dziko lino kumalima fodya wa mkulu wa chamba.

Aphunguwa avomerezana kuti kulima mbewuyi kuthandiza kuti dziko lino lidzipeza ndalama zochuluka.

Phungu wa ku m’mwera kwa Lilongwe a Peter Dimba ndi omwe anabweretsa nkhaniyi m’nyumbayi.

Kwa nthawi yaitali pakhala pali lingaliro loloreza ulimi wa chamba-wu omwe ambiri akhala akunena kuti uli ndi kuthekera kotengera chuma cha dziko lino patsogolo.

Asanakambirane nkuvomerezana izi aphunguwa , kupezeka ukulima mbewuyi umakhala mlandu omwe anthu ambiri akugwira nawo jele m’ndende zosiyanasiyana m’dziko muno.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *