Chakwera Wayamikira A Mpinganjira Kaamba Ka Chipatala

Wolemba: Noel Mkwaila, BLANTYRE

President Lazarus Chakwera wayamikira mkulu ochita malonda a Thom Mpinganjira pokhazikitsa chipatala chapamwamba chothana ndi nthenda ya cancer munzinda wa Blantyre chotchedwa International Blantyre Cancer Centre-IBCC.

A Chakwera ati izi zithandizira kwambiri ku nkhondo yolimbana ndi nthendayi pomwe aMalawi ena osauka amangodzifera popeza sangakwanitse kupita m’maiko ena monga India kukapeza thandizo.

Iwo ati akukhulupilira kuti dziko lino lidzakhala litayamba kuthandiza anthu odwala cancer mwalokha pofika 2030.

A Mpinganjira ati malingaliro omanga chipatalachi anawadzera, mkazi wawo atamwalira ku nthenda ya cancer zaka zisanu zapitazo ndipo akuzindikira bwino za zokhoma zomwe zilipo kaamba kakusowa kwa chipatalachi mdziko muno.

“Ndili ndi chimwemwe kwambiri kuti chipatalachi chatheka ndipo ndithokoze boma kaamba ka thandizo lomwe limapereka pa nthawi yomanga chipatalachi,” atero a Mpinganjira.

Chipatalachi chamangidwa ndi bungwe la Thomson and Barbra Foundation komanso abwenzi ena.

Pakadalipano, ndalama zoposa K9 billion ndi zomwe zagwira ntchito pa chipatalachi.

Related Posts

Mustag Chothia, Sulema Ismael Karim In Land scam

Land remains one area that Malawians know has been heavily abused, characterised by ownership wrangles, not to mention corruption, fueled Read more

AGHF Feeds Patients, Guardians At Mangochi District Hospital

A giving hand foundation is a local organisation working in various programs in Malawi. On Thursday the organization together with Read more

The Concerned Citizens Furious With Chizuma’s Stubbornness

The concerned citizens group which is advocating for sanity in civil service have vowed to take drastic measures in responding Read more

Mirece supports land reclamation bought by foreigners

Reverend Flywell Somanje…. this is the way to go A governance and human rights organization, the Millennium Information and Resource Read more

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

FDH Launch Islamic Banking Window