Chilima Alankhula Ku Mtundu Wa Amalawi Lachisanu

1 min read

Dr. Saulos Chilima ati Lachisanu likudzali alankhula ku mtundu wa Malawi ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko komanso mtsogoleri wa UTM pa zinthu zomwe zikuchitika m’dziko lino zomwe ndizofunikira.

M’neneri wa UTM, Frank Mwenifumbo watsimikiza izi ndipo wati izi zidzachitikira ku ofesi ya chipanichi ku Area 10 munzinda wa Lilongwe.

Pakadalipano, a Chilima apempha otsatira chipanichi komanso a Malawi kuti adekhe.

Lachisanu lapitali, Dr..Chilima adati anthu asayese kupusa kufatsa komwe adaonetsa pomwe dziko lino linkakonzekera chisankho cha mtsogoleri wa dziko mu June 2020.

Dr. Chilima alankhulanso patangotha masiku ochepa atakana kotheratu kuti sakudziwapo kanthu pa kuwaganizira kuti adachita za katangale ndi Zuneth Sattar.

You May Also Like

More From Author

+ There are no comments

Add yours