Diso La Ndale Likuona Patali Pomwe A Muluzi Akhululukidwa Milandu

Estimated read time 3 min read

50 + 1 Ndi nambala yomwe aliyense ali nayo mmaganizo mwake Maka Maka anzathu andalewa. Poganizila kuti nyengo yofuna kukopa a mphevu dyera kunthikofe yayandikira.

Inde poti ndale nkugwetsana zipani zakangalika kulimbitsa zipaninzawo mmadera osiyanasiya, posachedwapa tawona chipani cha afford chikukangalika kuchititsa misonkhano yake Madera osiyanasiyana, ponena akumati ndi misonkhano yachikondwerero kuti akwanitsa zaka zochuluka chikhazikitsireni chipani chawo. tinaona nkhwimbi la anthu linali kumeneko komanso tinamva mfundo zawo iwotu ulendo uno sakulabada za munthu koma mtsogoleri wawo a Enock chihana ayima paokha popeza iwo atopa kutsogoza atsogoleri ena omwe akalowa muboma sakuchita zomwe amalawi akufuna.
Diso la ndale layang’ana pa 50 +1 kuti kodi afford ngati imakanika popandala lamulori kuwina kodi pano pomwe 50+1 ali m’bwalo afford ingadutse? Tinene mosabitsa afford siyani kulota panganibe mgwilizano ndi chipani cha kumtima kwanu kuti mukhale m’boma kapena kuti muzapezeko unduna. Kupanda kutero Diso landale silikukuonani 2025.

KU DPP

Kumbali ya DPP chidwi cha Diso la ndale chagona pa chisankho chawo chomwe achititse chosankha mtsogoleli wachipani chawo. Kumeneku kuli anthu angapo omwe akupikisana, adadi tiwayiwale ndi munthu odekha iwo sangapangenso dala chibwana chofuna kuimira, pakadali pano akhala dala chete kufuna kuti asagawanitse chipani akanena kuti saimira kapena akasankhiratu munthu. Koma angakhale tikudziwa zofuna zawo koma kupanga chibwana chosiya Kondwani Nankhumwa pa udindo wawo juzakhala kutha kwa chipani ngati makatani. Ndalama ndi kutchuka ndizosiyana pandale, kabambe atha kukhala wa chuma koma mfundo za ndale alibe kumusankha iye ilo ndi bomba mwazitchera nokha, kumeneko kodwani nankhumwa ndiye jokala wanu. Iye atha kukhala opanda ndalama kuyerekeza ndi enawa koma ali ndi mfundo pa ndale, zili ndi inu kutola Jokala yu kapena ayi

MCP VS UTM

Mgwedegwede uli pakati pa zipani ziwilizi. Kodi atsogolele amalawi ndi ndani? Tinene mosabisa pano bomali ndi la mgwilizano Kaya mukwiya kapena ayi chifukwa munasokherana a zipani ziwirinu. Aliyense payekha anakanika mu 2019, munatenga bomali kamba ka malamulo chifukwa khoti linagamula kuti chisankho chinayendetsedwa mosasata malamulo. Chipani cha MCP mosabisa chakhala chikunena kuti iwo mtsogoleri wawo ndi Chakwela ndipo mosabisa UTM mtsogoleri wawo ndi Chilima, Koma chomwe sitikudziwa ndi chakuti mgwilizano wa Tonse ukhalapo? Ngati utakhalepo atsogolere ndani?

Mukuona kwa Diso la ndale chipani cha MCP chikuponyera mbedza kwa Kuya, zomwe zachitika lero pokhululukira a Bakili muluzi pa mlandu wawo ndi chizindikilo chimodzi kuti MCP ikufuna kuzakhala pa mgwilizano ndi UDF. Ndi akufuna kuzagwilitsa ntchito mwana wa amuluzi ngati wachiwiri wawo. Munthu wamba ngati inu ndi ine sungazimvetse koma ukakhala ndi diso la ndale uzimvetsa, Duso la ndale linayambabkuona izi kale kale tonse Italian muboma pomwe qmuluzi amatumizidwa kunja kuhaimira a chakwera, kenakom mkumano wawo pa namondwe wa Freddy. lero ndi lero boma kuzangozambatuka nkuneba kuti taunikira mulanduwu tawona kuti ulibe tsogolo. Zoona pa zaka 14 lero limenero kuona kuti mulandu wakuba 1.7 billion ulibe tsogolo.

Ndale nkutcherana ndiye Chipani cha UTM chikuyenera kusamala chifukwa chizazindiikira chili mu dzenje ngati sichikhala ndi Diso la ndale . A UTM sakudera nkhawa chifukwa chipani chonse chomwe chagwilizana ndi UDF sichinawinepo masankho. Ndipo MCP iziwe kuti pa ndale palibe mdani weniweni UTM NDI DPP atha kuzagwlizananso. Cholinga chofuna kugwersa MCP .

Kukhala chete kwa chilima kukudetsa nkhawa ambiri otsatila chipanichi ndipo akufunitsitsa atamva maganizo ake koma poti ndale nkutcherana UTM ndi utsogoleri wawo nawo palipo pomwe aponda mwala.

Andale samalani ndipo khalani ndi DISO LA NDALE

DR MWALE

More From Author

+ There are no comments

Add yours