Kalindo Wapempha Chakwera Achotse Ntchito Chizuma Masiku Okwana Asanu Ndi Awiri

Mkulu wa bungwe la Concerned Citizens and Timely Voices (CCTV) Bon Kalindo, wapempha mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera kuti ayimitse pa ntchito mkulu wa bungwe la Anti Corruption Bureau (ACB) Martha Chizuma.

`Pempholi likudza pomwe pa 7 April chaka chino, woweruza Geofry Nyirenda ku bwalo la mlandu la Mzuzu Magistrate, analamula nthambi ya apolisi ya Criminal Investigation Department mogwirizana ndi nthambi yozenga anthu milandu ya DPP kuti afufuze zokhudza mau a mkulu wa ACB omwe anthu amagawana pa masamba a mchezo.

Woweruzayi anapereka chigamulochi kutsatira a Frighton Phompho omwe ndi nzika ya dziko lino ndipo asumira mkulu wa ACB kuti kudzera mu mau awo omwe anthu akugawana pa masamba amchezo, anaphwanya malamulo okhudza ntchito yawo a corrupt practice poulula chinsisi cha ntchito yawo zomwe ati zikusephana ndi malamulo osunga chinsinsi.“`

Malingana ndi a Kalindo, kuyimitsa pa ntchito a Chizuma, kuthandiza kuti kafukufuku wa apolisi pa nkhaniyi ayende bwino ndikuti chilungamo pa milandu yomwe akuwaganizira chiwoneke.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *