Mchithunzi, Kantukule kulandira President Chakwera pa Kamuzu International Airport}.
Gulu lomwe likudzitchula kuti General Membership of Malawi Congress Party laonetsa kudabwa kuti President Lazarus Chakwera adasankha nduna yaza ntchito Vera Kantukule kuyang’anira dziko pomwe ankapita ku Mozambique m’mwezi wa April chaka chino chikhalirecho ndunayi siya MCP komanso ilibe udindo ulionse mchipanichi.
Iwo akuti a Chakwera akanatha kusankha amai ena mchipanichi omwenso ali nkuthekera pomwe ati pa ndale mtsogoleriyu adaphonya.
Izi ndi malinga ndi kalata yomwe gululi latulutsa pomwe latinso anthu ochulula omwe analembedwa ntchito ku nyumba ya boma {State House} ndi a mpingo wa Assemblies of God.
Kalatayi yomwe yasainidwa ndi m’neneri wake, Zinenani Magola komanso wapampando, Alex Major yatinso mamembalawa ndiokhudzidwa ndi zomwe adanena m’neneri wa MCP, Maurice Munthali kuti mtsonkhano waukulu wa chipanichi udzachitika mu 2024 osati 2023 zomwe akuti nzosemphana ndi malamulo awo.
“Tikupemphanso Chakwera kuti azikwanilitsa zomwe amayankhula komanso kumvera zomwe amalangizidwa,” yatero kalatayi.
M’neneri wa chipani cha MCP komanso wa President Chakwera, Anthony Kasunda sadayankhulepo pa kalatayi.
{
Read also: NBM plc supports MDF Sports Festival with K5.5 million
Read also: Linde Motel Cuts Workers Salaries By Half
Read also: RAILA Leads Mangochi District Hospital Cleanup and Patient Feeding Initiative

