Mike Baloni Wamangidwa Pomuganizira Kuti Wapha Mkazi Wake Mercy Jones

Ku Blantyre, apolisi amanga bambo wa zaka 45, Mike Baloni pomuganizira kuti wapha mkazi wake Mercy Jones.

M’neneri wa polisi ya Blantyre Peter Mchiza wauza Mzati kuti kutsatira kafukufuku wa apolisi apeza mpeni wakuthwa m’nyumba ya Baloni omwe akuganizira kuti adawugwiritsa ntchito pochitira chiwembuchi.

Mchiza wati pa 19 April chaka chino, apolisi adalandira uthenga woti ku dera lotchedwa Baluti mu nzindawu, kudapezeka thupi la mayi wina lomwe lidalibe mutu ndi miyendo.

Kutsatira kafukufuku, Mchiza wati achibale a malemuyu adazindikira kuti ndi m’bale wawo, komabe mwamunayu adakanika kuzindikira ndikuwanamiza apolisi kuti mkazi wake wapita ku mudzi kwawo ku Zomba.

Iye wati kafukufuku wa apolisi adapeza kuti zomwe bamboyu adanena zidali za bodza popeza achibale a mkaziyu atsimikiza kuti ku Zomba kulibe m’bale wawo.

Mchiza wati ngakhale zifukwa zomwe bamboyu waphera mkazi wake sizinadziwike, komabe anthu okhala moyandikana ndi bamboyu awuza apolisi kuti chiwembuchi chisanachitike, adawamva akukangana m’nyumba yawo.

Padakali pano apolisi ati thupi la malemuyu alipereka kwa abale awo kuti akaliyike m’manda, pamene woganiziridwayu akaonekera ku bwalo la mlandu pposachedwap

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *