Ndalama Zogula Magalimoto Ambiri Mwazitenga Kuti? Concerned Citizens Of Malawi

Gulu lina lotchedwa Concerned Citizens of Malawi lalembera kalata bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu m’dziko muno la Anti-Corruption Bureau (ACB) kuti lifufuze nduna ya za chuma, Simplex Chithyola Banda, komanso mwana wawo, Regina Chithyola, akuti pa chuma chambiri chomwe achipeza m’nthawi yochepa.

Poyankhula ndi Timveni online, Edward Kambanje, yemwe ndi wapampando wagululi, wati ndiodabwa ndi m’mene anthu awiriwa alemelera.

Kambanje, wati mwa chitsanzo, Regina yemwe ali ndi zaka 24, ali ndi chuma chochuluka pomwe iye sagwira ntchito.

“Ife tikudabwa kuti mwana wanduna-yi wazitenga kuti ndalama zogula ma galimoto apamwamba okwana makumi awiri,” watero Kambanje.

Kambanje wati a Chinthyola akuyenera kufotokoza bwino komwe akutenga ndalamazi.

Ndipo m’neneri wa bungwe la ACB, Egrita Mndala, watsimikiza kuti bungwe-li lalandira kalata yomwe gulu la Concerned Citizens lalembera bungwe-li.

Wolemba:Alex Batison & Johans Mumba

timveni online

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *