Tidkira Tsiku Lomwe Ayambe Kupanga Zipatso Zoyendera-CDEDI

Bungwe la Centre for Democracy and Economic Development initiatives-CDEDI lati lidikirabe tsiku lomwe nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka iyambe ntchito yake yopanga ziphaso(Passport).

Komabe mkulu wa bungweli,Sylvester Namiwa wati wokondwera ndi ganizo la nthambi yoona zolowa ndi kutuluka potsitsa mtengo wa e-passport.

Namiwa wati ngakhale ali wokondwa ndi kutsika mtengo wa chiphaso , iye wati ganizo lotsitsa mtengo wa chiphasochi limayenera kuchitika pa nthawi yomwe boma linathetsa mgwirizano wake ndi kampani ya Techno Brain.

Nthambi yoona zolowa ndi kutuluka yalengeza kuti ntchito yopanga ziphaso iyambiraso sabata ino.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *