ONYAMULA MAKALA AMUNJATA KU SALIMA

Apolisi ku Salima amanga bambo wa zaka 30, Yotamu Mapulanga pomuganizira kuti amazembetsa makala ndipo amulandanso galimoto yomwe ananyamulira makalawo ponena kuti inalibe kalata zoyenera.

M’neneri wa apolisi m’bomalo, Sub-Inspector Jacob Khembo wati apolisi alanda galimoto ya 15 ton ya mtundu wa Scania yomwe nambala yake ndi KK 7020, yomwe inali yodzadza ndi matumba a makala.

Sub-Inspector Khembo wati apolisi anagwira mkukuyu anthu ena atawatsina khutu koma pano ntchito yofufuza ili mkati kuti agwire anthu ena omwe athawa.

Mapulanga amachokera m’mudzi wa Chilipa, mfumu yaikulu Chimwala, m’boma la Mangochi.

Iye akawonekera ku bwalo zofufuza za apolisi zikatha.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *