Phungu Wa Nyumba Ya Malamulo Wamangidwa Atagunda Wa Traffic

Apolisi amanga phungu wa nyumba ya malamulo wa dera lakumpoto chakummawa kwa boma la Ntcheu, Arthur Chipungu pomuganizira kuti adagunda ndikuvulaza wa polisi wa pansewu yemwe akuti adalephera kumupatsa thandizo loyenera.

M’neneri wa polisi, Peter Kalaya wati mkuluyu wakhala akuthawathawa kwa masiku asanu ndi limodzi chichitikireni nkhani-yi Lachiwiri sabata yatha.

Kalaya wati amanga phungu-yu atadzipereka ekha ku likulu la polisi munzinda wa Lilongwe, komwe anabwera ndi loya wake.

Chipungu akumuganizira kuti adachita za chipongwezi pa malo a pakati pa bwalo la zamasewero la Bingu ndi Area 18 Interchange munzindawu.

Pakadalipano, Kalaya wati apolisi akusunga mkuluyu ku polisi ya Lingadzi ndipo akaonekera kubwalo la milandu mawa, Lachiwiri.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *