Sindingalowe UTM yomwe ili ndi aphungu anayi – Nankhumwa

1 min read

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) kumwera Kondwani Nankhumwa wanena mphekesera zoti akufuna kugulitsa chipanichi ku UTM kapena Malawi Congress Party (MCP).

A Nankhumwa amalankhula izi dzulo ku Lilongwe pa Mgona ground pomwe adachita msonkhano wa ndale.

Adayankha mphekesera zomwe zidamveka zoti akadzapambana kukhala Purezidenti wa DPP Nankhumwa alowa UTM kapena MCP.

Malinga ndi a Nankhumwa sangalowe UTM yomwe ili ndi aphungu anayi okha ku Nyumba ya Malamulo.

Adapitiliza kunena kuti iye ndi DPP ndipo sakuganiza zolowa chipani china chilichonse.

Malinga ndi a Nankhumwa ati adzapikisana nawo pa mpando wa utsogoleri kumsonkhanowu ndipo apambana ndi 95%.

You May Also Like

More From Author

+ There are no comments

Add yours