“`President Lazarus Chakwera wataya mlongo wawo Mirriam Chakwera yemwe wamwalira lero.
Mlembi wa atolankhani a President Anthony Kasunda walengeza za imfa ya mlongo wake wa Chakwera mwachidule.
A Kasunda adaonjeza kuti Chakwera wathetsa nthawi yomweyo zokambirana zake ndi anthu.
“Mtsogoleri wa dziko lino ayambiranso zokambirana zake ndi anthu akayika maliro a mlongo wawo, zomwe zikuyenera kuchitika pa Epulo 20 m’mudzi mwa Manase ku Mdika m’boma la Dowa,” adatero Kasunda.“`
Read also: Former Silver Strikers Captain has died
Read also: Malawi’s Asimenye Simwaka Disqualified from Commonwealth Games 400m
Read also: Papal Conclave Cuisine: A historical analysis of food, secrecy and symbolism

