Tichepese Mafuta A Galimoto Za Nduna–Watero M’neneri Wa Tonse Alliance

Yemwe amayankhulira mgwirizano wa Tonse, Kamuzu Chibambo wati mafuta a galimoto omwe nduna komanso alembi m’boma amalandira atsike kuchoka pa 2000 liters kufika pa mulingo osapyola 750 liters pamwezi ngati njira imodzi yotetezera chuma chadziko lino.

Chibambo, yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Peoples Transformation-PETRA walankhula izi pa msonkhano wa olemba nkhani munzinda wa Blantyre.

Iye watsindika kufunika kokhazikitsa kapena kutsatira mfundo zotukulira chuma kuti dziko lino lidzitha kukhala ndi ndalama zothetsera vuto lakusowa kwa ndalama zakunja.

Atakumana atsogoleri a Tonse miyezi yapitayo, Chibambo adauza a Malawi kuti adakambirana mfundo zothetsera mavuto a chuma omwe ayala mphasa m’dziko lino pakadalipano.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *