Ndondomeko Za Chuma Sizikuyendabwino–Mwanamveka

Chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) ndi chomwe chayamba kuyankhulapo pa ndondomeko ya za chuma ya mchaka cha 2024 mpaka 2025 yomwe inapelekedwa ku nyumba ya malamulo pa 23 February 2024.

Phungu wa dera la ku m’mwera kwa boma la Chiradzulu, yemwenso wasankhidwa ngati m’neneri wa Chipani cha DPP pa nkhani za chuma, Joseph Mwanavemkha wati boma lalephera kufotokoza bwino komwe lipeze ndalama zomwe liyendetsere ndondomeko ya za chumayi.

Malingana ndi Mwanavemkha, bungwe lotolela misonkho mdziko muno likuvutika ndi kale kutolela misonkho kamba kakuti chuma sichikuyenda bwino.

Mwanavemkha wati ndondomekoyi ipangitsa kuti ma business ambiri atsekedwe chifukwa cha ku chuluka kwa misonkho.

Iye wachenjezaso kuti dziko lino liyembekezere kuti chuma cha dziko lino chipitilira kukumana ndi mavuto kamba ka mikangano yomwe ilipo mmayiko akunja, ngozi zogwa mwadzidzidzi komanso kusowa kwa ndalama ya kunja.

Komabe, Mwanavemkha wati anthu akhale ndi chikhulupiliro kuti DPP ikhala ikubwereranso m’boma kudzapulumutsa anthu ku mavuto a zachuma omwe akukumana nawo chaka cha mawa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *