Malawi Freedom Network
Giving you daily news that rock the world

CHAKWERA NDI CHILIMA ANAPANGA MGWILIZANO OTI AZALAMULIRA ZAKA ZIWILI NDI MIYEZI 6 WINA ALIYESE

BREAKING NEWS; CHAKWERA NDI CHILIMA ANAPANGA MGWILIZANO OTI AZALAMULIRA ZAKA ZIWILI NDI MIYEZI 6 WINA ALIYESE

Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera ndi mlembi wachipani cha MCP Eisenhower Mkaka zulo anakhumudwisa akuluakulu ena achipani cha MCP atatulusa poyela mfundo zomwe Dr Lazarus Chakwera ndi Dr Saulos Chilima anagwilizana mene ankatenga boma muchaka cha 2019.

Awiliwa abwela poyela kamba koti Dr Saulos Chilima akuwonesa kuti sopano wayamba zamatukutuku pokonzekela kuzatenga boma kumathelo a mwezi wa December chaka chino kapena pa 1 January chaka cha 2023

Chakwera anati zipani za MCP ndi UTM zisanatenge boma zinayamba kukambilana mfundo yoti Dr Lazarus Chakwera azalamulile zaka kenako Dr Saulos Chilima nawo azalamulile zaka zina 5 mwatsoka chipani cha UTM chinakanisisa ponena kuti ndizinthu zakutali ndipo zamoyo siziziwika.

Chakwera anapitiliza kunena kuti zokambilana zoyamba zitalepheleka mbali ziwilizi zinagwilizana mfundo yoti iye azalamulile zaka ziwili ndimiyezi 6 kenako azasiyile Dr Saulos Chilima nawo kuti azalamulile zaka zina ziwili ndimiyezi 6 koma munthawiyo Vice President azachokela kuchipani cha MCP ndipo azakhala mlembi wachipanicho omwe ndi Eisenhower Mkaka.

Popitiliza nkhaniyi a Eisenhower Mkaka anawuza akuluakulu achipani cha MCP kuti mbali ziwilizi zitagwilizana mfundo yolamulira zaka ziwili ndi miyezi 6, anayitanisa ma Lawyer ndima Judge ena omwe anazasayinila panganoli.

“Bwanji simunatiwuze nthawi yonseyi” “eti..eti…inu” akuluakulu ena achipani cha MCP anamveka kung’ona chapansipansi zomwe zinachitisa.

Zokambila zinafika povuta kamba koti ma membala ena samagwilizana ndipanganoli ndipo amunisisa kuti Dr Lazarus Chakwera akathese mgwilizanowo

Anthuwa atelephela kumvana Dr Chakwera anayimisa kaye zokambilana kufikila sabata yamawa pomwe azagwilizane mfundo zingapo za nkhaniyi ndi nkhani zina.

Pakanali pano Dr Saulos Chilima wayamba kale kugula magalimoto ochuluka muchipani chake kamba akuziwa zoti kunja kwamuchela ndipo nthawi.

Leave a Comment

* By using this form you agree with the storage and handling of your data by this website.

This website uses cookies to improve your experience. We'll assume you're ok with this, but you can opt-out if you wish. Accept Read More