Gulu la Concerned Citizens of Malawi lalembera wapampando wabungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), Justice Annabel Mtalimanja kuti atule pansi udindo wake m’sanga.
Malingana ndi kalata ya gululi, utsogoleri wa Justice Mtalimanja uli ndi zofooka zambiri zomwe zili ndikuthekera kodzasokoneza zotsatira za chisankho cha chaka cha mawa.
Mwa zina, kalatayi yomwe yasainidwa ndi mtsogoleri wagululi, Edward Kambanje yati pali ubale waukulu pakati pa iye ndi chipani cha Malawi Congress (MCP) komanso kuti bungweli likukakamira Smartmatic ngakhale kuti mbali zokhudzidwa maka zipani zotsutsa boma zakhala zikukana izi.
“Udindo wa Justice Annabel Mtalimanja ukufunikira munthu yemwe ndioima payekha osati okhudzidwa ndi chipani chili chonse,” yatero mbali ina ya kalatayi.
Justice Mtalimanja sanayankhulepo, koma iwo akhala akuuza nyumba zofalitsa nkhani kuti akugwira ntchito motsatira malamulo a dziko lino.


MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!