Atatopa ndikudikira kuti boma komanso andale awakonzere msewu olumikiza maboma a Dedza ndi Salima kudzera ku dera la Kasumbu, anthu okhala m’madera a Mfumu Madzumbi Nakaona, Chiwamba ,Ndembo ndi nzoola m’dela la Mfumu yayikulu Kasumbu ku Dedza akupala okha ndi makasu msewu wotalika makilomita 12 omwe ndioipa kwambiri.
A Gulupu a Madzumbi atiuza kuti anaganiza zochita izi kaamba kakuti kwanthawi yaitali akhala akuvutika kwambiri popita ku msika kukagulitsa mbewu, komanso kukapeza zofunikira pa moyo wawo watsiku ndi tsiku.
Iwo atinso chifukwa china nchakuti msewu akupalawu ndi wachidule kuyerekeza ndikuzungulira ku boma la Dedza koyenda ma ola 9.
Mafumu ndi anthu kumeneko apempha akulu akulu kuti asiye kuwakumbukira nthawi ya chisankho yokha komanso kuthana mavuto omwe akukumana nawo.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!