Technical sub committee ya FAM yati mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Bullets Kalisto Pasuwa ndiye ali oyenera kukhala mphunzitsi watimu ya Flames mongogwilizila.
Izi zakambidwa dzulo ku Mpira Village ku Chiwembe munzinda wa Blantyre pomwe komitiyi imaunikira tsogolo la timu ya mpira wamiyendo ya dziko lino.
Matsiku apitawa bungwe la FAM linalengeza kuti agwilizana ndi mphunzitsi watimu ya Flames Mario Marian Marinica kuti saonjezelaso contract pomwe contract yake ikutha kumathero kwa mwezi uno.
Anthu okonda masewero mdziko muno akhala akuonesa kusakondwa ndi kaseweledwe ka timu ya Flames pansi pa Mario Marinica.