1001734645

Kamtukule walowa Chipani cha MCP

Wolemba: Racheal Julaye.

Nduna ya zokopa alendo Vera Kamtukule yalowa mchipani cha Malawi Congress.

Kamtukule akuchokera ku chipani Cha UTM chomwe chatuluka mu mgwilizano wa Tonse sabata zingapo zapitazo.

Polankhula atalandilidwa mchipanichi, Kamtukule ati iwo aganiza zolowa mchipanichi pofuna kuthandizana ndi President Chakwera kukweza Malawi.

Masiku apitawo Kamtukule anauza nyumba zina zoulutsa mau kuti iye akufuna kutumikila a Malawi ndipo kutuluka kwa chipani cha UTM mu mgwilizano wa Tonse sizikusintha ganizoli.

Oscar Taulo yemwe anali mlangizi wa za malamulo mchipani cha DPP naye walowa mchipani cha MCP.

More From Author

IMG 20240714 WA0069 300x217

Kamtukule faces controversy: Kaliati disowns Minister, analysts suggest political motives

Food12 300x198

Politics overshadows a conference to raise money for Ukraine

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Ella Brown

Project Manager

Darkness cannot drive out darkness; only light can do that. Hate cannot drive out hate: only love can do that.