Timu ya Premier Bet Dedza Dynamos yalengeza zakubwereranso kuchisa kwa katswiri wa kutsogola, Promise Kamwendo, yemwe anautsa mpungwe-mpungwe pa msika ogula ndi kugulitsa osewera m’dziko muno.
Izi zikudza kutsatira chigamulo cha bungwe la Football Association of Malawi (FAM) chomwe linapereka kuti katswiriyu akuyenera kubwerera ku timuyi kamba kosatsata ndondomeko.
Kamwendo wapanga nawo zokonzekera ku timuyi pamene ikuyembekezeka kusewera ndi timu ya Creck Sporting pa bwalo la Dedza mu ligi ya TNM kumapeto a sabatayi.
Katswiriyu ali ndi zigoli zisanu ndi chimodzi mu ligi ya TNM pamasewero 13 omwe anasewera.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!