Timu ya masewero a mpira wa miyendo ya dziko lino usiku wa lero ili ndi masewero a mtima bii pomwe ikhale ikukumana ndi timu ya Senegal.
Awa ndi masewero odzigulira malo ku mpikisano wa Afcon wa chaka cha mawa omwe ukachitikire m’dziko la Morocco.
Timu ya Malawi ikuyenera mwa njira iliyonse kupambana masewerowo kuti loto lake lokafika ku Morocco likhalepobe.
Pa masewero awiri omwe timuyi yasewera mu ndimeyi, Flames yagonja masewero onse.
Mphunzitsi wa timuyi Patrick Mabedi wati timu yakeyi itha kupambana masewerowa pokhapokha osewera ataikirapo mtima.
Matimuwa akakumana lero ku Senegal, akuyembekezeka kubwerezana lachiwiri likubwerali pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.
M’masewero a mu gulu lomweli, usiku wapitawu Burkina Faso yababada Burundi 4-1.