Mphunzitsi wa timu ya mpira wamiyendo ya dziko lino ya Flames, Patrick Mabedi, wati mwa njira ina ili yonse, timuyi ikuyenera kupeza chipambano pamasewero ake ndi Burkina Faso lachiwiri likudzali ku Bamako dziko la Mali.
Mabedi walankhula izi atangofika m’dziko la Mali komwe anyamata ake awongola minyewa komanso kuchita zokonzekera zoyamba za masewerowa, kuti timuyi idzigulire malo mu mpikisano wa Africa Cup of Nations (AFCON).
Mphunzitsiyu wati sakuyenera kumataya ma pointi kuti akhale ndi mwayi waukulu ochita bwino, potengera kuti ma timu ena m’gululi Senegal komanso Burkina Faso anafanana mphamvu pamasewero awo.
Mabedi, yemwenso ndi katswiri wakale otchinga kumbuyo mu timu ya Flames, walongosolanso kuti anali ndi nthawi younika zolakwika zomwe anyamata ake anachita pamasewero omwe anagonja 3-2 ndi Burundi, ndipo akuyembekeza chipambano pa masewerowa.
Ndipo, timu ya Burundi yomwe ili mugulu L yaitanitsa anyamata a Senegal mawa, lolemba, pa bwalo la Bingu nzinda wa Lilongwe.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!