Mphunzitsi wamkulu wa timu ya Kamuzu Barracks, Charles Kamanga, wadandaula kuti osewera ake ena akusewera ngati sakufuna.
Izi wayankhula kutsatira Kukhadzulidwa 2-0 ndi a nkhondo anzawo kuchokera ku Kaning’ina, Moyale Barracks.
Kamanga wati Ndizokhumudwitsa kumaona osewera ake akupereka zigoli zomwe zikumupatsa mafunso ngati mphunzitsi.
”Osewera ngati akusewera ali ndi china chake ku mtima, sangasewere mpira. Ndinene pano kuti pali osewera ena akusewera ngati akuchita kukakamizidwa zomwe ndizonkhumudwitsa kwambiri,” watero Kamanga.
Iye wati sangayankhule zambiri popeza ndizakuchipinda, komabe apangapo kanthu pamene atsala ndi masewero amodzi okha mu ligi ya TNM.
Kamuzu Barracks inayamba bwino ligiyi ndipo pomwe akapumira chigawo choyamba cha ligiyi nkuti ili panambala 4 ndimapointi 23.
Koma ng’ombe zayang’ana kungolo pomwe pakanali pano ali panambala 10, pomwe akwanitsa kupambana ka 8 kufananitsa mphamvu ka 13 ndikugonja ka 8 ndipo ali ndi mapointi 37.
Maloto oti akhoza kumaliza mkati mwa matimu 8 kuti apate mwayi osewera mu Airtel Top 8 chaka cha mawa athera m’mazira.
MALAWI
FREEDOM
NETWORK
United for Freedom, Justice and a Better Malawi
Airtel Money
0994095804
Mpamba
0881428759
FDH Bank
Acc No:
1400000670385NBS Bank
Acc No:
10118988Thank you for your support!