M’mawa wa lero lamulungu pa 1 December, 2024, His Excellency Prof Arthur Peter Mutharika ndi chipani chonse cha Democratic Progressive Party ( DPP) mchigawo chakummwera chikhala chikulowera Ku chigwa cha nsinje wa Shire.
Ulendowu wakonzedwa m’cholinga chokawadziwitsa anthu za kalembera wa mavote amene alinkati m’ma boma a Nsanje ndi Chikwawa kuphatikiza ma maboma ena monga Mangochi, Lilongwe komanso Mzimba.
Akulu-akulu a Chipani cha DPP, monga Mlembi Wamkulu Olemekezeka a Peter Mukhito, wachiwiri kwa mtsogoleri mchigawo chakummwera olemekezeka a Joseph Mwanamvekha MP, Mkulu okonza misonkhano m’chipani cha DPP olemekezeka a Sameer Suleman MP, Regional Governor Olemekezeka a Charles Mchacha MP komanso aphungu ndi ma khansala mchigawochi ndi amene akuyembekezeka kukalankhula m’malo onse amene mwakonzedwa misonkhano.