Chipani cha MCP chati chipani cha DPP ndichipani chabodza lotheratu chomwe chimangodziwa kunamiza a Malawi.
Izi zanenedwa kutsatira zomwe zayankhulidwa pamsonkhano wandale la Mulungu kwa Phwetekere mu mzinda wa Lilongwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha DPP chigawo chapakati Alfred Gangata kuti misewu yamakono yomwe ikumangidwa mu mzinda wa Lilongwe inayambidwa ndi chipani cha DPP ndipo MCP ikungomalizitsa chabe.
misewu yamakono yomwe ikumangidwa mu mzinda wa Lilongwe inayambidwa ndi chipani cha DPP watero Gangata
Mneneli wachipani cha MCP Jessie Kabwira wauza Nkhoma Synod Radio kuti chipani cha DPP chilibe mfundo zogwilika ndipo Gangata ndi munthu yemwe amangoyankhula poti dziko lino lili ndi ufulu wademokalase koma simunthu omutengera zoyankhula zake.
Malingana ndi a Kabwira misewu yonse yomwe ikumangidwa padakali pano mwini wake ndi MCP osati zomwe akunena a Gangata kaamba koti DPP ndichipani chomwe chimangodziwa kuba osati kutukula dziko lino.