Awa ndi mawu ochokera ku bungwe la Chewa Heritage Foundation (Chefo) lomwe layankhulapo pankhani yomwe ati inachitika kudera lina ku Monkey Bay m’boma la Mangochi kumene anamvetsedwa kuti gule wamkulu anamenya munthu mpaka kumwalira.
Poyankhulapo pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe, mkulu woona za mafumu, magule ndi miyambo ku bungweli a Lyson Banda ati uyu sadali gule wamkulu koma munthu woyesezera guleyu pofuna kupezapo mwayi ochita zoipa.
A Banda anaonjezeranso kuti gule wamkulu samatuluka chisawawa komanso samayenera kuyenda atanyamula zida zoopsa monga zikwanje komanso nkhwangwa.
M’mawu ake mfumu yaikulu Masumbankhunda yapempha adindo kuti agwiritse ntchito malamulo pomanga yemwe wachita izi ponena kuti asayipitse chikhalidwe chawo.