Mkulu wa malamulo m’dziko muno Thabo Chakaka Nyirenda ali m’dziko la Germany kusaka ndalama za amerika zokwana 543,000 zomwe zidasowa pomwe boma limafuna kugula feteleza
Chakaka Nyirenda wati ali kumeneko kulondoloza mapepala omwe athandizire pa kupezeka kwa ndalamazi
Boma la Malawi linabetsa ndalama zokwana K 750 million ku kampani ya Barkaat Foods Limited yomwe inkati igulitsa unduna wa zaulimi feteleza otsika mtengo