Sat. Apr 27th, 2024

Chipani UTM chati chiwonetsetsa kuti mfundo za mgwirizanowu zatsatiridwa

Chimodzi mwa zipani zomwe zili mu mgwirizano wa Tonse, cha UTM chati chiwonetsetsa kuti mfundo za mgwirizanowu zatsatiridwa.

Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM wayankhula izi pomwe kwadutsa zaka zinayi chichokereni pomwe zipani za UTM komanso MCP, mwa zina, zinapanga mgwirizano wa Tonse.

Mgwirizanowu unapangidwa pa 19 March mchaka cha 2020.

Poyankhula ndi MIJ Online, Kaliati wati chipanichi chili ndi chidwi chofuna kuona ngati ma membala a mgwirizanowu akwanilitse mfundo zomwe anagwirizana m’mbuyomu.

“Mu zaka zinayi zapitazi, ife ngati chipani cha UTM taphunzirapo zambiri mu mgwirizanowu ndipo tili ndi chidwi pofuna kuona mathero a mgwirizanowu, “watero Kaliati.

MIJ Online, inayesera kuyankhula ndi Eisenhower Mkaka mlembi wamkulu wa chipani cha MCP yemwe anati tiyankhule ndi mneneri wachipanichi Ezekiel Ching’oma yemwe sanayankhe lamya yathu.

Ndipo poyankhulapo pa nkhaniyi, katswiri pa ndale, Enerst Thindwa wati nzokayikitsa ngati mgwirizanowu upitilire kamba koti ma membala a zipani ziwiri zomwenso mzikuluzikulu akusemphana maganizo.

“Ubale wa atsogoleri awiri a zipani za UTM komanso MCP ukumawoneka kuti ulibwino, koma vuto ma membala a zipani zonse ziwiri akusemphana maganizo, ” watero Thindwa.

Posachedwapa, mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera, anadzudzula anthu omwe akufuna kubweretsa udani pakati pa iye komanso wachiwiri wake Saulos Chilima yemwe ndi mtsogoleri wa chipani cha UTM.

Pofika lero, pomwe kwatha zaka, mfundo zomwe zimamanga mgwirizanowu sizidziwikabe.

Related Posts
DPP Blues Rebels Brings Division In
DPP Blues Rebels Brings Division In

The way Charles Mchacha is castigating the Leader of Opposition in Parliament, Hon Kondwani Nankhumwa, is just testimony enough that Read more

Malawi business tycoon Simbi Phiri disassociates himself from forming up “Congress for Democrats”

Business Mogul Simbi Ashan Phiri who is Executive Chairman of Katho Civils has disassociated himself from social media rumours that Read more

Navicha appointed as a leader of opposition in parliament

Member of parliament for Thyolo Thava, Mary Thom Navicha has been recently appointed as a new leader of opposition following Read more

Jumah says it is possible to change Malawi in 10-15 years

By Vincent Gunde President and Commander in Chief of Muvi wa Chilungamo Revolutionary Party (MRP) Bantu Saunders Jumah, says it Read more

Other stories

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Ekhaya luxury Resort fully open