Tikuchosani Ku Bagamoyo Chaka Cha Mawa

Chipani cha DPP chati chikubweleraso m’boma chaka cha mawa kuti chiwombole anthu pa mavuto.

Mkulu owona zokopa anthu m’chipanichi a Everton Chimulirenji ayankhula izi la mulungu pa msonkhano omwe chipanichi chinachititsa ku Ntcheu.

A Chimulirenji ati a Malawi akudutsa mu nyengo zowawa kuphatikizapo njala ndi kukwera mitengo kwa zinthu.

Iwo ati chipanichi chakonzeka kuwaombola a Malawi pa mavutowa kaamba koti mayankho a Malawi ali ndi chipanichi.

Pa msonkhanowu, chipanichi chinalandiraso m’modzi mwa anthu omwe awonetsa chidwi chodzaimira pa mpando wa phungu wa chipanichi m’bomali a Mandela Ndilinde Gomeza.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *