Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM Patricia Kaliati sabata latha anauza Malawi and world news kuti chomwe iwo akudziwa ndi choti President wawo Saulos Klaus Chilima ndi yemwe adzatsogolere Tonse Alliance pa chisankho cha President chaka cha mawa.
Mu mgwirizanowu muli zipani za UTM, MCP, PP ndi zina.
Kaliati wayankhula izi pomwe chipani cha MCP chinabwera poyera kuti President Lazarus Chakwera ndiyemwe adzaimire chipanichi pa chisankhocho.